Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 10:13-15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Zitatero Mose analoza dziko lonse la Iguputo ndi ndodo yake, ndipo Yehova anachititsa mphepo yochokera kumʼmawa kuwomba padziko lonselo, masana onse ndi usiku onse. Mʼmawa kutacha mphepoyo inabweretsa dzombe. 14 Dzombelo linafika mʼdziko lonse la Iguputo nʼkufalikira mʼmadera onse adzikolo+ ndipo linawononga kwambiri.+ Dzombe lambiri ngati limeneli linali lisanagwepo nʼkale lonse ndipo silidzagwanso lambiri ngati limeneli. 15 Dzombelo linakuta nthaka yonse yamʼdzikolo ndipo dziko linachita mdima. Dzombelo linadya zomera zonse zamʼdzikolo ndi zipatso zonse zamʼmitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala, moti sipanatsale chobiriwira chilichonse mʼmitengo kapena mʼminda mʼdziko lonse la Iguputo.

Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena