-
Ekisodo 14:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ndiyeno mngelo wa Mulungu woona+ amene ankayenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka nʼkupita kumbuyo kwawo. Ndipo chipilala cha mtambo chija chinachoka kutsogolo nʼkukaima kumbuyo kwawo.+ 20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unkachititsa mdima, ndipo mbali ina unkawaunikira usiku.+ Choncho gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.
-