-
Oweruza 10:6-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Aisiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ mafano a Asitoreti, milungu ya ku Aramu,* milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya Aamoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Iwo anasiya Yehova ndipo sankamutumikira. 7 Zitatero, Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli moti anawapereka* kwa Afilisiti ndi kwa Aamoni.+ 8 Choncho, anthu amenewa anazunza ndi kupondereza kwambiri Aisiraeli chaka chimenecho. Kwa zaka 18, anapondereza Aisiraeli onse amene anali kumʼmawa kwa Yorodano, mʼdziko la Aamori limene linali ku Giliyadi.
-