7 Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu,+
Ndatsimikiza mtima.
Ndidzakuimbirani nyimbo ndi zipangizo zoimbira.
8 Dzuka, iwe ulemerero wanga.
Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.
Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.+
9 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+
Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+
10 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+
Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo.
11 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.
Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+