7 Simeyi ankanena kuti: “Choka! Choka! Munthu wa mlandu wa magazi ndiponso wopanda pake iwe! 8 Yehova wakubwezera mlandu wa magazi a nyumba ya Mfumu Sauli amene iwe unamulowa mʼmalo. Yehova wapereka ufumu mʼmanja mwa Abisalomu mwana wako. Ndipo tsoka lakugwera chifukwa uli ndi mlandu wa magazi!”+