-
Chivumbulutso 7:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Zimenezi zitatha, nditayangʼana ndinaona khamu lalikulu la anthu, amene palibe munthu aliyense amene anatha kuwawerenga, ochokera mʼdziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.+ 10 Iwo anapitiriza kufuula ndi mawu okweza akuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+
-