-
2 Mbiri 31:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Hezekiya anachita zimenezi ku Yuda konse ndipo anapitiriza kuchita zabwino, zoyenera komanso zokhulupirika pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21 Anagwira ndi mtima wake wonse ntchito iliyonse imene anaiyamba pofunafuna Mulungu wake, kaya ndi yokhudza utumiki wapanyumba ya Mulungu woona+ kapena Chilamulo, ndipo zinthu zinamuyendera bwino.
-