-
Yakobo 1:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Chifukwa ngati munthu amangomva mawu koma osachita,+ amafanana ndi munthu amene akudziyangʼanira nkhope yake pagalasi. 24 Iye amadziyangʼana nʼkuchokapo ndipo nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani. 25 Koma amene amayangʼanitsitsa mulamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu ndipo amapitiriza kuliyangʼanitsitsa, adzakhala wosangalala ndi zimene akuchita+ chifukwa chakuti si munthu amene amangomva nʼkuiwala, koma amene amachita zimene wamvazo.
-