Miyambo 2:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Koma anthu oipa adzachotsedwa padziko lapansi+Ndipo achinyengo adzazulidwamo.+ Miyambo 25:4, 5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Yengani siliva nʼkuchotsa zonse zosafunika,Ndipo yense adzatuluka woyengeka bwino.+ 5 Chotsani woipa pamaso pa mfumu,Ndipo mpando wake wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chilungamo.+ Ezekieli 22:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 “Iwe mwana wa munthu, kwa ine nyumba ya Isiraeli yakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo. Onse ali ngati kopa,* tini, chitsulo ndi mtovu zimene zili mungʼanjo. Iwo akhala ngati zinthu zimene zimatsalira akayenga siliva.+
4 Yengani siliva nʼkuchotsa zonse zosafunika,Ndipo yense adzatuluka woyengeka bwino.+ 5 Chotsani woipa pamaso pa mfumu,Ndipo mpando wake wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chilungamo.+
18 “Iwe mwana wa munthu, kwa ine nyumba ya Isiraeli yakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo. Onse ali ngati kopa,* tini, chitsulo ndi mtovu zimene zili mungʼanjo. Iwo akhala ngati zinthu zimene zimatsalira akayenga siliva.+