1 Samueli 30:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Davide anali ndi nkhawa kwambiri chifukwa anthu ankakambirana zoti amuponye miyala. Anthuwo ankafuna kuchita zimenezi chifukwa anakwiya kwambiri ndi kutengedwa kwa ana awo aamuna ndi aakazi. Koma Davide anakhulupirira Yehova Mulungu wake ndipo anapeza mphamvu.+ Salimo 62:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 62 Ndithudi, ndikuyembekezera* Mulungu modekha. Chipulumutso changa chimachokera kwa iye.+ Yesaya 30:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Chifukwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Woyera wa Isiraeli, wanena kuti: “Mukabwerera kwa ine nʼkukhala odekha, mudzapulumuka.Mudzakhala amphamvu mukakhala odekha komanso mukasonyeza kuti mukundidalira.”+ Koma inu simunafune.+ Maliro 3:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Ndi bwino kuti munthu akhale chete*+ nʼkumayembekezera chipulumutso cha Yehova.+
6 Davide anali ndi nkhawa kwambiri chifukwa anthu ankakambirana zoti amuponye miyala. Anthuwo ankafuna kuchita zimenezi chifukwa anakwiya kwambiri ndi kutengedwa kwa ana awo aamuna ndi aakazi. Koma Davide anakhulupirira Yehova Mulungu wake ndipo anapeza mphamvu.+
15 Chifukwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Woyera wa Isiraeli, wanena kuti: “Mukabwerera kwa ine nʼkukhala odekha, mudzapulumuka.Mudzakhala amphamvu mukakhala odekha komanso mukasonyeza kuti mukundidalira.”+ Koma inu simunafune.+