7Choncho amuna a ku Kiriyati-yearimu anabweradi nʼkutenga Likasa la Yehova ndipo anakaliika mʼnyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Ndiyeno anasankha* Eliezara mwana wake kuti azilondera Likasa la Yehova.
6 Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali mʼdera la Yuda kukatenga Likasa la Mulungu woona, Yehova, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Pa Likasa limeneli, anthu amaitanirapo dzina lake.