-
2 Mbiri 6:41, 42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
41 Inu Yehova Mulungu nyamukani mulowe mʼmalo oti mupumeko,+ inuyo komanso Likasa limene mumasonyezera mphamvu zanu. Ansembe anu, inu Yehova Mulungu, avale chipulumutso ndipo okhulupirika anu asangalale chifukwa cha ubwino wanu.+ 42 Inu Yehova Mulungu, musakane wodzozedwa wanu.+ Kumbukirani chikondi chanu chokhulupirika chimene munasonyeza Davide mtumiki wanu.”+
-