11 Ukadzamwalira nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa yako, mmodzi wa ana ako,+ akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+ 12 Iye ndi amene adzandimangire nyumba+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+