8 Pa nthawi imeneyo tinalanda dziko la mafumu awiri a Aamori+ amene ankakhala mʼdera la Yorodano, kuyambira mʼchigwa cha Arinoni mpaka kuphiri la Herimoni.+ 9 (Phiri limeneli Asidoni ankalitchula kuti Sirioni, pamene Aamori ankalitchula kuti Seniri.)