-
Ekisodo 14:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja, ndipo kutatsala pangʼono kucha nyanjayo inayamba kubwerera mʼmalo mwake. Pamene Aiguputo ankathawa kuti madziwo asawapeze, Yehova anakankhira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+ 28 Madzi amene anabwererawo anamiza magaleta ankhondo, asilikali apamahatchi ndi gulu lonse lankhondo la Farao, amene analondola Aisiraeli mʼnyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+
-