-
2 Samueli 7:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga.+ 9 Ine ndidzakhala nawe kulikonse kumene ungapite,+ ndipo ndidzagonjetsa adani ako onse pamaso pako.+ Ndidzachititsa kuti dzina lako lidziwike+ ngati mmene zimakhalira ndi anthu otchuka mʼdzikoli.
-