-
Ezekieli 34:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko ena nʼkuzibweretsa mʼdziko lawo. Ndidzazidyetsa mʼmapiri a ku Isiraeli,+ mʼmphepete mwa mitsinje komanso pafupi ndi malo onse amʼdzikolo kumene kumakhala anthu. 14 Nkhosazo ndidzazidyetsera mʼmalo a msipu wabwino ndipo malo amene zizidzadya msipu adzakhala kumapiri ataliatali a ku Isiraeli.+ Kumeneko zizidzagona pansi mʼmalo abwino kwambiri odyetserako ziweto+ ndipo zizidzadya msipu wabwino kwambiri mʼmapiri a ku Isiraeli.
-