-
Mateyu 26:59-61Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
59 Ndiyeno ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* ankafunafuna umboni wabodza kuti anamizire Yesu mlandu nʼcholinga choti amuphe.+ 60 Koma sanaupeze ngakhale kuti kunabwera mboni zambiri zabodza.+ Patapita nthawi, kunabwera mboni zina ziwiri 61 nʼkunena kuti: “Munthu ameneyu ananena kuti, ‘Ndikhoza kugwetsa kachisi wa Mulungu nʼkumumanganso mʼmasiku atatu.’”+
-