-
Genesis 9:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke ndipo mudzaze dziko lapansi.+ 2 Chamoyo chilichonse chapadziko lapansi, chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga, chilichonse chokwawa padziko lapansi, ndi nsomba zonse zamʼnyanja, zidzapitiriza kukuopani. Tsopano ndapereka zonsezi mʼmanja mwanu.*+
-