-
Aroma 2:6-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Iye adzaweruza aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+ 7 Adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene akupitirizabe kuchita zabwino.+ Anthu amenewa akuyesetsa kupeza ulemerero, ulemu ndi moyo wosawonongeka. 8 Koma anthu amene amakonda mikangano, satsatira choonadi komanso amachita zosalungama, Mulungu adzawasonyeza mkwiyo wake.+
-