7 Musadzinamize, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+ 8 Chifukwa amene akufesa nʼcholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera mʼthupi lakelo, koma amene akutsatira mzimu wa Mulungu adzakolola moyo wosatha kuchokera ku mzimuwo.+