-
1 Akorinto 9:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda, kuti ndithandize Ayuda.+ Kwa anthu otsatira Chilamulo ndinakhala ngati wotsatira Chilamulo kuti ndithandize anthu otsatira chilamulo, ngakhale kuti sinditsatira Chilamulo.+ 21 Kwa anthu amene sayendera Chilamulo ndinakhala ngati wosayendera Chilamulo, kuti ndithandize anthu osayendera Chilamulo. Ndinachita zimenezi ngakhale kuti ndimatsatira malamulo a Mulungu komanso lamulo la Khristu.+ 22 Kwa ofooka ndinakhala wofooka, kuti ndithandize ofooka.+ Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti ndiyesetse mmene ndingathere kupulumutsa ena.
-