-
1 Samueli 2:22-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Pa nthawiyi Eli anali atakalamba kwambiri koma anamva zonse zimene ana ake ankachitira+ Aisiraeli onse. Anamvanso kuti ankagona ndi akazi amene ankatumikira pakhomo la chihema chokumanako.+ 23 Ndipo iye ankawauza kuti: “Mukuchitiranji zimenezi? Chifukwatu zimene anthu onse akundiuza zokhudza inu ndi zoipa zokhazokha. 24 Musatero ana anga, chifukwa nkhani zimene ndikumva, zimene anthu a Yehova akunena, si zabwino. 25 Munthu akachimwira mnzake, munthu wina akhoza kumuchonderera kwa Yehova,* koma akachimwira Yehova,+ angamupempherere ndi ndani?” Koma anawo sankamvera bambo awo ndipo tsopano Yehova anali atatsimikiza mtima kuti awaphe.+
-