-
1 Samueli 22:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako Sauli anauza asilikali othamanga amene anali atamuzungulira kuti: “Iphani ansembe a Yehova chifukwa ali kumbali ya Davide! Iwo ankadziwa kuti Davide akuthawa, koma sanandiuze!” Komabe atumiki a mfumuwo sanafune kupha ansembe a Yehova. 18 Ndiyeno mfumu inauza Doegi+ kuti: “Iwe, ipha ansembewa!” Nthawi yomweyo Doegi wa ku Edomu+ anapha ansembewo. Tsiku limenelo anapha amuna 85 ovala efodi wa nsalu.+
-
-
1 Mafumu 2:29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada kuti: “Pita ukamuphe!”
-