41 Ndiyeno Sauli anauza Yehova kuti: “Inu Mulungu wa Isiraeli, tiyankheni kudzera mwa Tumimu!”+ Atatero, Yonatani ndi Sauli anasankhidwa ndipo anthuwo anaoneka kuti alibe mlandu. 42 Kenako Sauli anati: “Chitani maere+ pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Zitatero, maerewo anagwera Yonatani.