16 Davide atamaliza kukwera phiri lija,+ anapeza Ziba+ mtumiki wa Mefiboseti+ akumudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu awiri okhala ndi zishalo atanyamula mikate 200, makeke 100 a mphesa, makeke 100 a zipatso zamʼchilimwe ndiponso mtsuko waukulu wa vinyo.+