-
Genesis 39:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Mkaziyo ankalankhula ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, koma iye sanamvere zoti agone pambali pake kapena kuti agone naye. 11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumba kuti akagwire ntchito yake, ndipo mʼnyumbamo munalibe antchito ena. 12 Choncho mkaziyo anagwira malaya a mnyamatayo nʼkumuuza kuti: “Ugone nane basi!” Koma mnyamatayo anangovula malayawo nʼkuwasiya mʼmanja mwa mkaziyo nʼkuthawira panja.
-
-
Miyambo 7:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Nzeru uiuze kuti: “Ndiwe mchemwali wanga,”
Ndipo kumvetsa zinthu ukutche “mʼbale wanga,”
-