-
2 Samueli 20:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndiyeno panali munthu wina wosokoneza dzina lake Sheba,+ mwana wamwamuna wa Bikiri,+ wafuko la Benjamini. Iye analiza lipenga la nyanga ya nkhosa nʼkunena kuti: “Ife Davide tilibe naye ntchito ndipo sitingapatsidwe cholowa kuchokera kwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu* yake!”+
-
-
2 Samueli 20:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Nthawi yomweyo, mayi wanzeruyo anapita nʼkukalankhula ndi anthu onse, ndipo anthuwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri nʼkuuponya kwa Yowabu. Zitatero, Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anthu onse anachoka kumzindawo nʼkupita kwawo.+ Yowabu nayenso anabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu.
-