-
Rute 1:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Koma Rute anati: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, chifukwa kumene inu mupite inenso ndipita komweko ndipo kumene mugone inenso ndigona komweko. Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.+ 17 Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri ngati chinachake kupatulapo imfa chingandisiyanitse ndi inu.”
-