-
Numeri 23:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako Balamu ananena ndakatulo yakuti:+
“Balaki mfumu ya Mowabu wandibweretsa kuno kuchokera ku Aramu,+
Kuchokera kumapiri akumʼmawa kuti:
‘Bwera, udzanditembererere Yakobo.
Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+
8 Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere?
Ndipo ndingathe bwanji kuitanira tsoka anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka?+
-
-
Machitidwe 5:38, 39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Choncho mmene zinthu zilili apapa, ndikukuuzani kuti asiyeni anthu amenewa musalimbane nawo. Chifukwa ngati zolinga zawo kapena ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali. 39 Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu, simungathe kuwaletsa.+ Ndipo mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”+
-