15 Misundu ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti, “Tipatseni! Tipatseni!”
Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta
Ndiponso zinthu 4 zimene sizinena kuti, “Ndakhuta!” Zinthu zake ndi izi:
16 Manda,+ mimba yosabereka,
Nthaka yopanda madzi
Komanso moto umene sunena kuti, “Ndakhuta!”