-
1 Mafumu 21:8-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu nʼkuwadinda ndi chidindo cha Ahabu.+ Kenako anatumiza makalatawo kwa akulu+ ndi anthu olemekezeka amumzinda umene Naboti ankakhala. 9 Mʼmakalatawo analembamo kuti: “Uzani anthu kuti asale kudya ndipo Naboti mumuike kutsogolo kwa anthu onse. 10 Ndiyeno mupeze anthu awiri opanda pake adzakhale kutsogolo kwake nʼkupereka umboni wotsutsana naye.+ Adzanene kuti, ‘Iwe wanyoza Mulungu ndi mfumu!’+ Kenako mukamutulutse kunja nʼkumuponya miyala kuti afe.”+
11 Choncho amuna a mumzinda umene Naboti ankakhala, akulu ndi anthu olemekezeka amumzindawo, anachita mogwirizana ndi zimene zinali mʼmakalata amene Yezebeli anawatumizira.
-
-
Yeremiya 38:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Akalonga anauza mfumu kuti: “Chonde lamulani kuti munthu uyu aphedwe+ chifukwa akufooketsa asilikali amene atsala mumzinda uno komanso anthu onse, powauza mawu amenewa. Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.” 5 Mfumu Zedekiya inawayankha kuti: “Taonani! Iye ali mʼmanja mwanu, ndipo palibe chilichonse chimene ndingachite kuti ndikuletseni.”
-