-
Deuteronomo 15:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Muzimupatsa mowolowa manja zimene akufunazo,+ ndipo musamamupatse* zinthuzo monyinyirika. Mukamachita zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita ndi ntchito zanu zonse.+ 11 Mʼdziko lanu mudzapitirizabe kupezeka anthu osauka.+ Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti, ‘Muzikhala owolowa manja kwa mʼbale wanu wovutika komanso wosauka mʼdziko lanu.’+
-