Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 26:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Komatu zimenezi ndi kambali kakangʼono chabe ka zochita zake,+

      Ndipo tangomva kunongʼona kwapansipansi kwa mphamvu zake.

      Ndiye ndi ndani amene angamvetse mabingu ake amphamvu?”+

  • Salimo 40:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Inu Yehova Mulungu wanga,

      Mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa+

      Ndipo mumatiganizira.+

      Palibe angafanane ndi inu.

      Nditati ndilankhule kapena kunena za zodabwitsazo,

      Zingakhale zochuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+

  • Mlaliki 8:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndiyeno ndinaganizira ntchito yonse ya Mulungu woona, ndipo ndinazindikira kuti anthu sangamvetse zimene zimachitika padziko lapansi pano.+ Ngakhale anthu atayesetsa bwanji sangathe kuzimvetsa. Ngakhale atanena kuti ndi anzeru kwambiri ndipo zonsezi akuzidziwa, sangathebe kuzimvetsa.+

  • Aroma 11:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake nʼzozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukire njira zake?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena