-
2 Samueli 19:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Koma Barizilai anauza mfumu kuti: “Kodi masiku a moyo wanga atsala angati kuti ndipite ku Yerusalemu pamodzi ndi mfumu? 35 Panopa ndili ndi zaka 80.+ Kodi ndingasiyanitse chabwino ndi choipa? Kodi ine mtumiki wanu ndingamve kukoma kwa zakudya ndi zakumwa? Nanga ndingathenso kumvetsera nyimbo za amuna ndi akazi oimba?+ Ndiye ine mtumiki wanu ndikulemetseni chifukwa chiyani mbuyanga mfumu?
-