8 Pa nthawi imeneyo Solomo anasonkhanitsa+ akulu a Isiraeli, atsogoleri a mafuko ndiponso atsogoleri a nyumba za makolo a Aisiraeli.+ Anabwera kwa Mfumu Solomo ku Yerusalemu kuti akatenge likasa la pangano la Yehova ku Mzinda wa Davide,+ komwe ndi ku Ziyoni.+