Salimo 62:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Komanso chikondi chokhulupirika ndi chanu, inu Yehova,+Chifukwa inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+ Mlaliki 11:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Mnyamata iwe, sangalala pa nthawi imene uli wachinyamata, ndipo mtima wako usangalale masiku a unyamata wako. Uzichita zimene mtima wako ukufuna ndipo uzipita kumene maso ako akukutsogolera. Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza* pa zinthu zonsezi.+ Mateyu 12:36, 37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu+ pa mawu aliwonse opanda pake amene iwo amalankhula. 37 Chifukwa ndi mawu ako udzaweruzidwa kuti ndiwe wolungama ndipo ndi mawu akonso udzaweruzidwa kuti ndiwe wolakwa.” Machitidwe 17:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ mwachilungamo dziko lonse lapansi, kudzera mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”+ 2 Akorinto 5:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chifukwa aliyense wa ife adzaonekera kumpando woweruzira milandu wa Khristu, kuti alandire mphoto yake mogwirizana ndi zimene anachita ali mʼthupi, kaya zabwino kapena zoipa.+ 1 Timoteyo 5:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Machimo a anthu ena amadziwika kwa anthu, ndipo amaweruzidwa nthawi yomweyo. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pakapita nthawi.+
12 Komanso chikondi chokhulupirika ndi chanu, inu Yehova,+Chifukwa inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+
9 Mnyamata iwe, sangalala pa nthawi imene uli wachinyamata, ndipo mtima wako usangalale masiku a unyamata wako. Uzichita zimene mtima wako ukufuna ndipo uzipita kumene maso ako akukutsogolera. Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza* pa zinthu zonsezi.+
36 Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu+ pa mawu aliwonse opanda pake amene iwo amalankhula. 37 Chifukwa ndi mawu ako udzaweruzidwa kuti ndiwe wolungama ndipo ndi mawu akonso udzaweruzidwa kuti ndiwe wolakwa.”
31 Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ mwachilungamo dziko lonse lapansi, kudzera mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”+
10 Chifukwa aliyense wa ife adzaonekera kumpando woweruzira milandu wa Khristu, kuti alandire mphoto yake mogwirizana ndi zimene anachita ali mʼthupi, kaya zabwino kapena zoipa.+
24 Machimo a anthu ena amadziwika kwa anthu, ndipo amaweruzidwa nthawi yomweyo. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pakapita nthawi.+