38 Chifukwa ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu,+ 39 msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.