-
1 Mafumu 5:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo wakuti: “Ndamva uthenga wanu. Ndichita zonse zimene mukufuna ndipo ndikupatsani mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ya junipa.*+ 9 Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni nʼkupita nayo kunyanja, ndipo ndidzaimanga pamodzi ngati phaka nʼkuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze. Kenako akaimasula ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Malipiro ake mudzandipatsa chakudya cha banja langa.”+
-