20 Kuchokera pamene dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa,+ ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu wake,+ zikuonekera mʼzinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.