-
Ezekieli 22:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndidzakusonkhanitsani pamodzi ngati mmene amasonkhanitsira siliva, kopa, chitsulo, mtovu ndi tini mungʼanjo kuti azikolezere moto nʼkuzisungunula. Ndidzachita zimenezi nditakwiya komanso mwaukali ndipo ndidzakukolezerani moto nʼkukusungunulani.+ 21 Ndidzakusonkhanitsani pamodzi nʼkukukolezerani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo mudzasungunuka mumzindawo.+ 22 Mofanana ndi siliva amene amamusungunulira mungʼanjo, inenso ndidzakusungunulirani mumzindawo. Choncho mudzadziwa kuti ine Yehova ndadzakukhuthulirani mkwiyo wanga.’”
-