-
Ekisodo 15:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Choncho anthu anayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Timwa chiyani?” 25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anamusonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko mʼmadzi moti madziwo anakhala okoma.
Pamalo amenewo Mulungu anawapatsa lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo kumeneko anawayesa.+
-
-
Deuteronomo 8:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 musakalole kuti mtima wanu ukayambe kunyada+ nʼkukuchititsani kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo,+ 15 amene anakuyendetsani mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni, zinkhanira ndiponso nthaka youma yopanda madzi. Iye anachititsa kuti madzi atuluke pamwala wolimba,+
-
-
Yesaya 43:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Kodi simukuchizindikira?
-