-
Machitidwe 8:32, 33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Mawu a mʼMalemba amene ankawerengawo anali akuti: “Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa. Ndipo mofanana ndi mwana wa nkhosa amene wangokhala chete pamene akufuna kumumeta ubweya, sanatsegule pakamwa pake.+ 33 Pamene ankamuchititsa manyazi, sanamuchitire zachilungamo.+ Ndi ndani angafotokoze mwatsatanetsatane mʼbadwo wa makolo ake? Chifukwa moyo wake wachotsedwa padziko lapansi.”+
-