32 Anthuwo anatenganso amuna ena awiri, amene anali zigawenga, kuti akawaphe limodzi ndi Yesu.+ 33 Ndiyeno atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamukhomerera pamtengo limodzi ndi zigawenga zija. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+