16 Ahazi+ mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya. 2 Ahazi anayamba kulamulira ali ndi zaka 20 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+