-
Luka 4:17-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ndiyeno anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anatambasula mpukutuwo nʼkupeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18 “Mzimu wa Yehova* uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu osauka. Anandituma kudzalengeza za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina komanso zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale pa ufulu,+ 19 ndi kudzalalikira za chaka chovomerezeka kwa Yehova.”*+ 20 Atatero anapinda mpukutuwo nʼkuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndipo anakhala pansi. Maso a anthu onse amene anali mʼsunagogemo anali pa iye nʼkumamuyangʼanitsitsa. 21 Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+
-
-
Machitidwe 26:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ndipo ndidzakupulumutsa kwa anthu awa komanso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutumiza+ 18 kuti ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mumdima+ nʼkuwapititsa kowala+ ndiponso kuwachotsa mʼmanja mwa Satana+ nʼkuwapititsa kwa Mulungu. Ukachite zimenezi kuti machimo awo akhululukidwe+ nʼkulandira cholowa pamodzi ndi oyeretsedwa chifukwa chondikhulupirira.’
-