-
1 Mafumu 16:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli mʼchaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda ndipo analamulira zaka 12. Ku Tiriza analamulirako zaka 6. 24 Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri ndi matalente* awiri asiliva ndipo anamanga mzinda paphiripo. Mzindawo anaupatsa dzina lakuti Samariya*+ lomwe linali dzina la Semeri, mwiniwake* wa phirilo.
-