-
2 Mbiri 27:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Yotamu+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 2 Yotamu ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Uziya bambo ake,+ kungoti sanachite makani nʼkukalowa mʼkachisi wa Yehova.+ Koma anthu ankachitabe zoipa.
-