-
Deuteronomo 13:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 “Pakati panu pakapezeka mneneri kapena wolosera za mʼtsogolo pogwiritsa ntchito maloto nʼkukupatsani chizindikiro kapena kulosera china chake, 2 ndipo chizindikiro kapena zimene analoserazo zachitikadi, kenako iye nʼkunena kuti, ‘Tiyeni titsatire milungu ina,’ milungu imene simukuidziwa, ‘ndipo tiitumikire,’ 3 musamvere mawu a mneneriyo kapena woloserayo,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukuyesani+ kuti adziwe ngati mumakonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.+
-