35 ‘Ndidzateteza mzindawu+ ndipo ndidzaupulumutsa chifukwa cha ineyo+
Ndiponso chifukwa cha mtumiki wanga Davide.’”+
36 Ndiyeno mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri nʼkukapha asilikali 185,000. Anthu podzuka mʼmawa, anangoona kuti onse ndi mitembo yokhayokha.+